Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 21:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Tsopano m’masiku a Davide kunagwa njala+ zaka zitatu zotsatizana. Choncho Davide anafunsira kwa Yehova, ndipo Yehova anamuuza kuti: “Sauli pamodzi ndi nyumba yake ali ndi mlandu wa magazi chifukwa anapha Agibeoni.”+

  • Miyambo 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa,+

  • Miyambo 8:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Kuopa Yehova kumatanthauza kudana ndi zoipa.+ Ndimadana ndi kudzikweza, kunyada,+ njira yoipa ndiponso pakamwa ponena zopotoka.+

  • Zekariya 5:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ine ndatumiza mpukutuwo kuti ukalowe m’nyumba ya munthu wakuba ndi m’nyumba ya munthu wolumbira mwachinyengo m’dzina langa.+ Mpukutuwo upita kukakhala m’nyumba mwake n’kuwonongeratu nyumbayo, matabwa ake ndi miyala yake.’”+

  • Zekariya 8:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Musamakonzerane ziwembu mumtima mwanu kuti muonetsane tsoka+ ndipo musamakonde kulumbira monama.+ Pakuti zinthu zonsezi ine ndimadana nazo,’+ watero Yehova.”

  • Malaki 3:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Anthu inu ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni.+ Sindidzazengereza kupereka umboni+ wotsutsa amatsenga,+ achigololo,+ olumbira monama+ komanso ochita chinyengo pa malipiro a munthu waganyu.+ Sindidzazengereza kupereka umboni wotsutsa anthu ochitira chinyengo mkazi wamasiye,+ mwana wamasiye*+ ndiponso opondereza alendo.+ Anthu amenewa sakundiopa,”+ watero Yehova wa makamu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena