7 Tembenukani ndi kulowera kudera lamapiri la Aamori+ ndi anthu oyandikana nawo onse okhala ku Araba,+ kudera lamapiri,+ ku Sefela, ku Negebu,+ m’mbali mwa nyanja,+ m’dziko la Akanani+ ndi ku Lebanoni+ mpaka kumtsinje waukulu wa Firate.+
40 Choncho Yoswa anapha anthu a m’dera lonse la mapiri,+ anthu a ku Negebu,+ a ku Sefela,+ ndi a m’madera otsetsereka+ pamodzi ndi mafumu awo onse. Iye anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka,+ ndipo anapha chamoyo chilichonse*+ monga mmene Yehova Mulungu wa Isiraeli analamulira.+
8 Dzikoli linkaphatikizapo dera lamapiri, dera la Sefela, chigwa cha Araba, malo otsetsereka, chipululu, ndi Negebu.+ Limeneli linali dziko la Ahiti, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi.+ Mafumu awo anali awa: