Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 23:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Sindidzawathamangitsa pamaso pako m’chaka chimodzi, kuti dzikolo lingakhale bwinja ndi kuti zilombo zakutchire zingachuluke ndi kukuvutitsa.+

  • Numeri 33:55
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 55 “‘Koma ngati simukawapitikitsa anthu onsewo,+ ndithu amene mukasiyewo adzakhala ngati zitsotso m’maso mwanu, ndiponso ngati minga yokulasani m’nthiti mwanu. Ndithu adzakusautsani m’dziko limene mudzakhalamo.+

  • Deuteronomo 7:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Yehova Mulungu wako adzakankhira mitundu imeneyi kutali ndi iwe, kuichotsa pamaso pako pang’onopang’ono.+ Sadzakulola kuifafaniza mofulumira, kuopera kuti zilombo zakutchire zingakuchulukire ndi kukuwononga.

  • Yoswa 23:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 dziwani kuti Yehova Mulungu wanu adzaleka kuwapitikitsa pamaso panu.+ Iwo adzakhala ngati msampha ndiponso ngati khwekhwe kwa inu.+ Adzakhalanso ngati zokubayani* m’mbali mwanu komanso ngati zitsotso m’maso mwanu, kufikira mutatheratu padziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+

  • Oweruza 1:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Fuko la Efuraimu nalonso silinapitikitse Akanani amene anali kukhala ku Gezeri, moti Akananiwo anakhalabe pakati pawo ku Gezeriko.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena