Ekisodo 23:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Asakhale m’dziko lako, kuti asakuchimwitse pamaso panga. Ukatumikira milungu yawo, umenewo udzakhala msampha kwa iwe.”+ Numeri 33:55 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 55 “‘Koma ngati simukawapitikitsa anthu onsewo,+ ndithu amene mukasiyewo adzakhala ngati zitsotso m’maso mwanu, ndiponso ngati minga yokulasani m’nthiti mwanu. Ndithu adzakusautsani m’dziko limene mudzakhalamo.+ Deuteronomo 20:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Mukawawononge kuti asakakuphunzitseni kuchita zinthu zawo zonse zonyansa zimene achitira milungu yawo, kuti mungachimwire Yehova Mulungu wanu.+ Oweruza 1:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 Ana a Benjamini sanapitikitse Ayebusi amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ moti Ayebusiwo akukhalabe ndi ana a Benjamini m’Yerusalemu kufikira lero.+
33 Asakhale m’dziko lako, kuti asakuchimwitse pamaso panga. Ukatumikira milungu yawo, umenewo udzakhala msampha kwa iwe.”+
55 “‘Koma ngati simukawapitikitsa anthu onsewo,+ ndithu amene mukasiyewo adzakhala ngati zitsotso m’maso mwanu, ndiponso ngati minga yokulasani m’nthiti mwanu. Ndithu adzakusautsani m’dziko limene mudzakhalamo.+
18 Mukawawononge kuti asakakuphunzitseni kuchita zinthu zawo zonse zonyansa zimene achitira milungu yawo, kuti mungachimwire Yehova Mulungu wanu.+
21 Ana a Benjamini sanapitikitse Ayebusi amene anali kukhala m’Yerusalemu,+ moti Ayebusiwo akukhalabe ndi ana a Benjamini m’Yerusalemu kufikira lero.+