22 Ndiye zinali kuchitika kuti, pa tsiku lankhondo panalibe munthu aliyense mwa anthu amene anali ndi Sauli ndi Yonatani, amene anali ndi lupanga+ kapena mkondo m’manja mwake. Koma Sauli+ yekha ndi mwana wake Yonatani ndi amene anali ndi zida.
50 Choncho Davide, mwa kugwiritsa ntchito gulaye ndi mwala, anali wamphamvu kuposa Mfilisiti. Iye anamukantha ndi kumupha, ndipo m’manja mwa Davide munalibe lupanga.+