Oweruza 7:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Ndipo magulu atatuwo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ ndi kuphwanya mitsuko ikuluikulu ija. Atatero ananyamulanso miyuni ndi dzanja lawo lamanzere ndipo malipenga anali m’dzanja lawo lamanja, n’kuyamba kufuula kuti: “Nkhondo ya Yehova+ ndi ya Gidiyoni!” 1 Samueli 17:47 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 47 Ndipo mpingo wonsewu udziwa kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena mkondo,+ chifukwa Yehova ndiye mwini nkhondo,+ moti apereka anthu inu m’manja mwathu.”+ 1 Samueli 17:50 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 50 Choncho Davide, mwa kugwiritsa ntchito gulaye ndi mwala, anali wamphamvu kuposa Mfilisiti. Iye anamukantha ndi kumupha, ndipo m’manja mwa Davide munalibe lupanga.+ Salimo 44:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Pakuti iwo sanatenge dzikolo chifukwa cha lupanga lawo,+Ndipo si mkono wawo umene unawabweretsera chipulumutso.+Koma chinabwera ndi dzanja lanu lamanja,+ mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,Chifukwa munakondwera nawo.+ Zekariya 4:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo,+ kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa makamu.
20 Ndipo magulu atatuwo analiza malipenga a nyanga ya nkhosa+ ndi kuphwanya mitsuko ikuluikulu ija. Atatero ananyamulanso miyuni ndi dzanja lawo lamanzere ndipo malipenga anali m’dzanja lawo lamanja, n’kuyamba kufuula kuti: “Nkhondo ya Yehova+ ndi ya Gidiyoni!”
47 Ndipo mpingo wonsewu udziwa kuti Yehova sapulumutsa ndi lupanga kapena mkondo,+ chifukwa Yehova ndiye mwini nkhondo,+ moti apereka anthu inu m’manja mwathu.”+
50 Choncho Davide, mwa kugwiritsa ntchito gulaye ndi mwala, anali wamphamvu kuposa Mfilisiti. Iye anamukantha ndi kumupha, ndipo m’manja mwa Davide munalibe lupanga.+
3 Pakuti iwo sanatenge dzikolo chifukwa cha lupanga lawo,+Ndipo si mkono wawo umene unawabweretsera chipulumutso.+Koma chinabwera ndi dzanja lanu lamanja,+ mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,Chifukwa munakondwera nawo.+
6 Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo,+ kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa makamu.