Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 43:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndiyeno bambo awo Isiraeli anawauza kuti: “Chabwino, ngati ndi choncho,+ chitani izi: Tengani zinthu zamtengo wapatali za dziko lino m’matumba anu, mukam’patse munthuyo monga mphatso.+ Tengani mafuta a basamu+ pang’ono, uchi+ pang’ono, mafuta onunkhira a labidanamu, khungwa la utomoni wonunkhira,+ mtedza wa pisitasho, ndi zipatso za amondi.+

  • Ekisodo 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Choncho nditsikira kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo,+ ndi kuwatulutsa m’dzikolo, n’kuwalowetsa m’dziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ndiwalowetsa m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperizi, Ahivi, ndi Ayebusi.+

  • Deuteronomo 32:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Anapitiriza kumuyendetsa pamapiri a dziko lapansi,+

      Moti anadya zokolola za m’minda.+

      Anapitirizanso kumudyetsa uchi wochokera m’thanthwe,+

      Ndi mafuta ochokera m’mwala wa nsangalabwi.+

  • Miyambo 24:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Mwana wanga, idya uchi chifukwa ndi wabwino, ndipo uchi wotsekemera wochokera pazisa za njuchi uuike m’kamwa mwako.+

  • Mateyu 3:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Koma Yohane ameneyu, anali kuvala chovala chaubweya wa ngamila+ ndi lamba wachikopa+ m’chiuno mwake. Chakudya chake chinali dzombe+ ndi uchi.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena