Ekisodo 3:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Kenako mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye pakati pa chitsamba chaminga+ chimene chinali kuyaka moto. Atachiyang’anitsitsa, anaona kuti chitsamba chamingacho chikuyaka, koma sichikupsa. Ekisodo 23:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 “Tsopano ndikukutumizira mngelo+ wokutsogolera kuti akuteteze m’njira ndi kukakulowetsa m’dziko limene ndakukonzera.+ Ekisodo 23:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Pakuti mngelo wanga adzakutsogolera ndi kukulowetsa m’dziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawafafaniza ndithu.+ Yoswa 5:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Tsiku lina Yoswa ali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo anaona mwamuna wina+ ataima potero patsogolo pake, ali ndi lupanga m’dzanja lake.+ Pamenepo Yoswa anayandikira munthuyo ndi kumufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?”
2 Kenako mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye pakati pa chitsamba chaminga+ chimene chinali kuyaka moto. Atachiyang’anitsitsa, anaona kuti chitsamba chamingacho chikuyaka, koma sichikupsa.
20 “Tsopano ndikukutumizira mngelo+ wokutsogolera kuti akuteteze m’njira ndi kukakulowetsa m’dziko limene ndakukonzera.+
23 Pakuti mngelo wanga adzakutsogolera ndi kukulowetsa m’dziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawafafaniza ndithu.+
13 Tsiku lina Yoswa ali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo anaona mwamuna wina+ ataima potero patsogolo pake, ali ndi lupanga m’dzanja lake.+ Pamenepo Yoswa anayandikira munthuyo ndi kumufunsa kuti: “Kodi uli kumbali yathu kapena kumbali ya adani athu?”