Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 35:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Umu ndi mmene Rakele anamwalirira, ndipo anamuika m’manda ali m’njira popita ku Efurata, komwe ndi ku Betelehemu.+

  • Oweruza 19:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Tsopano masiku amenewo, mu Isiraeli munalibe mfumu.+ Ndiyeno Mlevi wina anakhala kwa kanthawi m’dera lamapiri lakutali kwambiri la Efuraimu.+ Patapita nthawi, anatenga mkazi wa ku Betelehemu,+ ku Yuda, kukhala mdzakazi wake.+

  • Rute 1:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Tsopano zinachitika kuti, m’masiku amene oweruza+ anali atsogoleri, m’dzikomo munagwa njala.+ Ndiyeno munthu wina anasamuka ku Betelehemu+ wa ku Yuda kukakhala m’dziko la Mowabu+ monga mlendo. Anasamuka ndi mkazi wake ndi ana ake awiri aamuna.

  • Mika 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Iwe Betelehemu Efurata,+ ndiwe mzinda waung’ono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda.+ Komabe mwa iwe+ mudzatuluka munthu amene adzakhale wolamulira mu Isiraeli,+ amene adzachite chifuniro changa. Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira nthawi zoyambirira, wakhala alipo kuyambira masiku akalekale.+

  • Mateyu 2:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Yesu atabadwa ku Betelehemu+ wa Yudeya m’masiku a mfumu Herode,*+ okhulupirira nyenyezi+ ochokera kumadera a kum’mawa anabwera ku Yerusalemu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena