Rute 2:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndipo pa nthawi ya chakudya Boazi anaitana Rute kuti: “Tabwera kuno udzadye mkate+ ndiponso uziusunsa mu vinyo wowawasayu.” Choncho Rute anadzakhala pansi limodzi ndi okololawo, ndipo Boazi anali kum’patsira mbewu zokazinga,+ iye n’kumadya moti anakhuta mpaka zina kutsala. 1 Samueli 17:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Kenako Jese anauza Davide mwana wake kuti: “Tenga tirigu wokazinga+ uyu wokwana muyezo umodzi wa efa ndi mitanda ya mkate 10, upite nazo mofulumira kwa abale ako kumsasa. 2 Samueli 17:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 anabweretsa makama, mabeseni, ziwiya zadothi, tirigu, balere, ufa,+ tirigu wokazinga,+ nyemba zikuluzikulu,+ mphodza+ ndi tirigu wowamba.
14 Ndipo pa nthawi ya chakudya Boazi anaitana Rute kuti: “Tabwera kuno udzadye mkate+ ndiponso uziusunsa mu vinyo wowawasayu.” Choncho Rute anadzakhala pansi limodzi ndi okololawo, ndipo Boazi anali kum’patsira mbewu zokazinga,+ iye n’kumadya moti anakhuta mpaka zina kutsala.
17 Kenako Jese anauza Davide mwana wake kuti: “Tenga tirigu wokazinga+ uyu wokwana muyezo umodzi wa efa ndi mitanda ya mkate 10, upite nazo mofulumira kwa abale ako kumsasa.
28 anabweretsa makama, mabeseni, ziwiya zadothi, tirigu, balere, ufa,+ tirigu wokazinga,+ nyemba zikuluzikulu,+ mphodza+ ndi tirigu wowamba.