Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 32:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+

      Pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo lidzaterereka poyenda,+

      Pakuti tsiku la tsoka lawo layandikira,+

      Ndipo zowagwera zikufika mofulumira.’+

  • 1 Samueli 24:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu,+ ndipo Yehova andibwezerere,+ koma dzanja langali silidzakukhudzani.+

  • 1 Samueli 25:38
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 38 Patapita masiku 10, Yehova anakantha+ Nabala ndipo anafa.

  • Salimo 94:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 94 Inu Yehova, Mulungu wobwezera anthu oipa,+

      Inu Mulungu wobwezera anthu oipa, walani!+

  • Salimo 94:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Iye adzawabwezera zoipa zawo,+

      Ndipo adzawakhalitsa chete mwa kuwadzetsera masoka okonza okha.+

      Yehova Mulungu wathu adzawakhalitsa chete.+

  • Aroma 12:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Okondedwa, musabwezere choipa,+ koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Pakuti Malemba amati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine, watero Yehova.”+

  • Yuda 9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Koma pamene Mikayeli+ mkulu wa angelo+ anasemphana maganizo+ ndi Mdyerekezi ndipo anakangana naye za mtembo wa Mose,+ sanayese n’komwe kumuweruza ndi mawu onyoza,+ m’malomwake anati: “Yehova akudzudzule.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena