18 Choncho Davide anathawa ndi kupulumuka,+ moti anafika kwa Samueli ku Rama.+ Atafika kumeneko anasimbira Samueli zonse zimene Sauli anam’chitira. Kenako Davide ndi Samueli anachoka ndi kupita kukakhala ku Nayoti.+
22Choncho Davide anachoka kumeneko+ ndi kuthawira+ kuphanga+ la Adulamu.+ Abale ake ndi nyumba yonse ya bambo ake anamva zimenezo, ndipo ananyamuka kumutsatira.