Genesis 33:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Chonde, landirani mphatso yokufunirani mafuno abwinoyi kuchokera kwa ine,+ chifukwa Mulungu wandikomera mtima, ndipo wandipatsa chilichonse.”+ Anamuumirizabe mpaka analandira mphatsoyo.+ 2 Mafumu 5:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Kenako iye pamodzi ndi gulu lake lonse anabwerera kwa munthu wa Mulungu woona+ uja. Anaima pamaso pake n’kunena kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti, padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu kupatula ku Isiraeli kokha.+ Ndiye landirani mphatso+ kuchokera kwa ine mtumiki wanu.” Miyambo 11:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Pali amene amapatsa mowolowa manja, komabe zinthu zake zimawonjezeka.+ Palinso amene safuna kupatsa ena zinthu zoyenera kuwapatsa, koma amangokhala wosowa.+ Miyambo 18:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Mphatso ya munthu imam’tsegulira khomo lalikulu,+ ndipo imakam’fikitsa ngakhale pamaso pa anthu olemekezeka.+ Machitidwe 20:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwira ntchito molimbika chomwechi,+ muthandize ofookawo,+ ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka+ kuposa kulandira.’”
11 Chonde, landirani mphatso yokufunirani mafuno abwinoyi kuchokera kwa ine,+ chifukwa Mulungu wandikomera mtima, ndipo wandipatsa chilichonse.”+ Anamuumirizabe mpaka analandira mphatsoyo.+
15 Kenako iye pamodzi ndi gulu lake lonse anabwerera kwa munthu wa Mulungu woona+ uja. Anaima pamaso pake n’kunena kuti: “Tsopano ndadziwa ndithu kuti, padziko lonse lapansi kulibenso kwina kumene kuli Mulungu kupatula ku Isiraeli kokha.+ Ndiye landirani mphatso+ kuchokera kwa ine mtumiki wanu.”
24 Pali amene amapatsa mowolowa manja, komabe zinthu zake zimawonjezeka.+ Palinso amene safuna kupatsa ena zinthu zoyenera kuwapatsa, koma amangokhala wosowa.+
16 Mphatso ya munthu imam’tsegulira khomo lalikulu,+ ndipo imakam’fikitsa ngakhale pamaso pa anthu olemekezeka.+
35 M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwira ntchito molimbika chomwechi,+ muthandize ofookawo,+ ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweretsa chimwemwe chochuluka+ kuposa kulandira.’”