Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 27:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 “‘Ngati munthu watenga munthu mnzake, nyama kapena munda wake n’kuupatula kuti ukhale woyera kwa Yehova kwamuyaya,* kapena akapereka munthuyo, nyama kapena munda kwa Mulungu kuti auwononge,+ sungagulitsidwe kapena kuwomboledwa.+ Munthu, nyama kapena munda umenewo ndi wopatulika koposa. Zimenezi ndi za Yehova.

  • Yoswa 7:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Ana a Isiraeli sadzathanso kulimbana ndi adani awo.+ Iwo azingothawa kwa adani awo, chifukwa iwonso akhala zinthu zoyenera kuwonongedwa. Sindidzakhalanso nanu kufikira mutachotsa pakati panu zinthu zoyenera kuwonongedwazo.+

  • 1 Samueli 13:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Kenako Sauli anati: “Bweretsani kuno nsembe yopsereza ndi nsembe zachiyanjano.” Pamenepo iye anapereka nsembe yopserezayo.+

  • Miyambo 11:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kodi kudzikweza kwafika? Ndiye kuti manyazinso afika.+ Koma nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.+

  • Miyambo 14:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Pali njira yooneka ngati yowongoka kwa munthu,+ koma mapeto ake ndi imfa.+

  • Miyambo 21:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Munthu amene amadzikuza akapsa mtima, amatchedwa wodzikuza, wonyada ndi wodzitama.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena