Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 15:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Ndikumva chisoni+ kuti ndinaika Sauli kukhala mfumu. Iye watembenuka,+ wasiya kunditsatira, ndipo sakumvera mawu anga.”+ Samueli anavutika maganizo kwambiri ndi nkhani imeneyi+ moti anafuulira Yehova usiku wonse.+

  • 1 Samueli 15:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Poyankha Samueli anati: “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza+ ndi nsembe zina kuposa kumvera mawu a Yehova? Taona! Kumvera+ kuposa nsembe,+ ndipo kumvetsera mosamala kuposa mafuta+ a nkhosa zamphongo.

  • 1 Samueli 15:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Pakuti kupanduka+ n’chimodzimodzi ndi tchimo la kuwombeza,+ ndipo kuchita zinthu modzikuza n’chimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito mphamvu zamatsenga ndiponso aterafi.+ Popeza iwe wakana mawu a Yehova,+ iyenso wakukana kuti usakhalenso mfumu.”+

  • Salimo 37:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Khala chete pamaso pa Yehova,+

      Ndipo umuyembekezere ndi mtima wako wonse.+

      Usapse mtima ndi aliyense amene zinthu zikumuyendera bwino,+

      Munthu amene akukwaniritsa zolinga zake zoipa.+

  • Miyambo 11:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Kodi kudzikweza kwafika? Ndiye kuti manyazinso afika.+ Koma nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.+

  • Miyambo 13:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Chifukwa cha kudzikuza, munthu amangoyambitsa mavuto,+ koma anthu amene amakhala pamodzi n’kumakambirana amakhala ndi nzeru.+

  • Miyambo 21:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Munthu amene amadzikuza akapsa mtima, amatchedwa wodzikuza, wonyada ndi wodzitama.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena