14 Ndiye Isiraeli anati: “Pita ukaone ngati abale ako ali bwino limodzi ndi nkhosa. Kenako ubwere udzandiuze.”+ Chotero, anamuuza kuti anyamuke kuchigwa cha Heburoni+ ndipo iye analowera ku Sekemu.
18 Magawo 10 awa a mkaka* ukapatse mtsogoleri wa gulu la anthu 1,000.+ Ukafufuzenso kuti abale ako ali bwanji,+ ndipo akakupatse chizindikiro chosonyeza kuti ali bwino.”