4 Chifukwa cha kukhulupirika kwa Davide,+ Yehova Mulungu wake anam’patsa nyale+ mu Yerusalemu mwa kukweza mwana wake pambuyo pake, ndiponso kuchititsa kuti Yerusalemu akhalepobe.+
19 Koma Yehova sanafune kuwononga ufumu wa Yuda+ chifukwa cha Davide mtumiki wake,+ pakuti anamulonjeza kuti adzam’patsa nyale+ nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake.