Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 7:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Choncho dalitsani+ nyumba ya mtumiki wanu kuti ikhazikike pamaso panu mpaka kalekale.+ Pakuti inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa mwalonjeza, ndipo madalitso anu akhale panyumba ya mtumiki wanu mpaka kalekale.”+

  • 2 Samueli 14:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Tsopano banja lonse landiukira ine mtumiki wanu ndipo aliyense akunena kuti, ‘Bweretsa wopha m’bale wakeyo+ kuti timuphe chifukwa cha moyo wa m’bale wake amene anamupha,+ ndipo tiwononge wolandira cholowayo!’ Tsopano anthuwa adzazimitsa makala anga onyeka otsalawo, kuti pasakhale wosunga dzina la mwamuna wanga kapena mbewu yake yotsala padziko lapansi.”+

  • 1 Mafumu 15:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Chifukwa cha kukhulupirika kwa Davide,+ Yehova Mulungu wake anam’patsa nyale+ mu Yerusalemu mwa kukweza mwana wake pambuyo pake, ndiponso kuchititsa kuti Yerusalemu akhalepobe.+

  • 2 Mafumu 8:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Koma Yehova sanafune kuwononga ufumu wa Yuda+ chifukwa cha Davide mtumiki wake,+ pakuti anamulonjeza kuti adzam’patsa nyale+ nthawi zonse, iyeyo ndi ana ake.

  • Luka 1:69
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 69 Iye watikwezera ife nyanga*+ yachipulumutso m’nyumba ya mtumiki wake Davide,

  • Machitidwe 15:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 ‘Zimenezi zikadzatha ndidzabwerera ndi kumanganso nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso malo ogumuka a nyumbayo ndi kuiimikanso.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena