-
Yoswa 15:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Kuchokera pamenepo, anapitirira mpaka kuchigwa cha mwana wa Hinomu,+ kumalo otsetsereka otchedwa Yebusi+ kum’mwera, kutanthauza Yerusalemu.+ Anapitirirabe mpaka pamwamba pa phiri loyang’anizana ndi chigwa cha Hinomu, limene lili kumadzulo kwa chigwacho. Phirilo lili kumpoto kwa chigwa cha Arefai,+ kumapeto kwa chigwacho.
-