15 Mfumu Solomo inaitana anthu ogwira ntchito yokakamiza+ kuti adzamange nyumba ya Yehova,+ nyumba yake, Chimulu cha Dothi,*+ khoma+ lozungulira Yerusalemu, ndiponso mizinda ya Hazori,+ Megido,+ ndi Gezeri.+
24 Mwana wamkazi wa Farao+ anachoka ku Mzinda wa Davide+ n’kukakhala kunyumba yake imene Solomo anam’mangira. Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamanga Chimulu cha Dothi.*+
27 Iye anaukira mfumu pa chifukwa ichi: Solomo anamanga Chimulu cha Dothi*+ ndiponso anatseka mpata umene unali pampanda wa Mzinda wa Davide bambo ake.+
5 Kuwonjezera apo, iye analimba mtima n’kumanga makoma onse a mpanda amene anali ogumuka.+ Anamanga nsanja+ pamwamba pa mpandawo ndipo kunja kwake anamangako mpanda wina.+ Anakonzanso Chimulu cha Dothi*+ cha mu Mzinda wa Davide ndipo anapanga zida+ zambiri ndi zishango.+