9 Davide anayamba kukhala m’malo okhala mumpanda wolimba kwambiri, ndipo anawatcha Mzinda wa Davide. Iye anayamba kumanga malo onsewo kuyambira ku Chimulu cha Dothi*+ mpaka mkati.
24 Mwana wamkazi wa Farao+ anachoka ku Mzinda wa Davide+ n’kukakhala kunyumba yake imene Solomo anam’mangira. Panali pa nthawi imeneyi pamene Solomo anamanga Chimulu cha Dothi.*+
27 Iye anaukira mfumu pa chifukwa ichi: Solomo anamanga Chimulu cha Dothi*+ ndiponso anatseka mpata umene unali pampanda wa Mzinda wa Davide bambo ake.+