12 Kenako anatulutsa mwana+ wa mfumu uja. Atatero anamuveka chisoti chachifumu+ n’kuika mpukutu wa Chilamulo cha Mulungu pamutu pake.+ Chotero anamulonga ufumu+ n’kumudzoza.+ Ndiyeno anayamba kuwomba m’manja+ n’kumanena kuti: “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”+