24 Dzina lanu+ likhale lokhulupirika ndi lokwezeka+ mpaka kalekale. Anthu anene kuti, ‘Yehova wa makamu+ Mulungu wa Isiraeli,+ ndiye Mulungu wa Isiraeli,’+ ndipo nyumba ya mtumiki wanu Davide ikhalitse pamaso panu.+
11 Inu Yehova, ukulu,+ mphamvu,+ kukongola,+ ulemerero,+ ndi ulemu+ ndi zanu, chifukwa zinthu zonse zakumwamba ndi za padziko lapansi ndi zanu.+ Ufumu+ ndi wanu, inu Yehova, ndinunso Wokwezeka monga mutu pa onse.+