Ekisodo 22:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 “Usatemberere Mulungu+ kapena kutemberera mtsogoleri amene ali pakati pa anthu ako.+ 1 Samueli 17:43 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 43 Choncho iye anafunsa Davide kuti: “Kodi ine ndine galu+ kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Atatero, anatemberera Davide m’dzina la milungu yake.+ Miyambo 1:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 “Anthu osadziwa inu, kodi mukufuna kukhalabe osadziwa mpaka liti?+ Inu onyoza, mukufuna kukhalabe onyoza mpaka liti?+ Ndipo opusa inu, mudana ndi kudziwa zinthu mpaka liti?+ Miyambo 26:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Mbalame imakhala ndi chifukwa chothawira, ndiponso namzeze* amakhala ndi chifukwa choulukira. Momwemonso temberero silibwera popanda chifukwa chenicheni.+ Mlaliki 10:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Ngakhale m’chipinda chako, usanenere mfumu zoipa,+ ndipo m’zipinda zimene umagona usanenere zoipa aliyense wolemera,+ chifukwa cholengedwa chouluka chikanena mawu ako ndipo chinachake chokhala ndi mapiko chikaulula zimene wanena.+ Machitidwe 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Pamenepo Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Pakuti Malemba amati, ‘Wolamulira wa anthu a mtundu wako usamunenere zachipongwe.’”+
43 Choncho iye anafunsa Davide kuti: “Kodi ine ndine galu+ kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Atatero, anatemberera Davide m’dzina la milungu yake.+
22 “Anthu osadziwa inu, kodi mukufuna kukhalabe osadziwa mpaka liti?+ Inu onyoza, mukufuna kukhalabe onyoza mpaka liti?+ Ndipo opusa inu, mudana ndi kudziwa zinthu mpaka liti?+
2 Mbalame imakhala ndi chifukwa chothawira, ndiponso namzeze* amakhala ndi chifukwa choulukira. Momwemonso temberero silibwera popanda chifukwa chenicheni.+
20 Ngakhale m’chipinda chako, usanenere mfumu zoipa,+ ndipo m’zipinda zimene umagona usanenere zoipa aliyense wolemera,+ chifukwa cholengedwa chouluka chikanena mawu ako ndipo chinachake chokhala ndi mapiko chikaulula zimene wanena.+
5 Pamenepo Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Pakuti Malemba amati, ‘Wolamulira wa anthu a mtundu wako usamunenere zachipongwe.’”+