11 Iye anawauza kuti: “Izi ndi zimene mfumu yokulamuliraniyo izidzafuna kwa inu:+ Idzatenga ana anu+ kuti azikayenda m’magaleta*+ ake ndi kukwera pamahatchi*+ ake, ndipo ena mwa ana anuwo azidzathamanga patsogolo pa magaleta ake.+
7 Solomo anali ndi nduna 12 mu Isiraeli yense, zomwe zinkabweretsa chakudya kwa mfumu ndi banja lake lachifumu. Nduna iliyonse inali ndi udindo wobweretsa chakudya kwa mwezi umodzi pachaka.+