17 Nthawi ndi nthawi anali kugula galeta lochokera ku Iguputo pamtengo wa ndalama zasiliva 600. Hatchi anali kuigula pamtengo wa ndalama zasiliva 150. Umu ndi mmene mafumu onse a Ahiti ndi mafumu a ku Siriya+ anali kuchitira. Mafumuwa anali kugwiritsa ntchito amalondawo pogula zinthuzo.