-
Nehemiya 1:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Chonde, tsegulani maso anu ndi kutchera khutu+ kuti mumve pemphero la ine mtumiki wanu+ limene ndikupemphera pamaso panu lero. Usana ndi usiku+ ndikupempherera atumiki anu, ana a Isiraeli. Pochita zimenezi ndikuvomereza+ machimo+ a ana a Isiraeli amene tinakuchimwirani. Tonse tinachimwa, ine pamodzi ndi nyumba ya bambo anga.+
-