9 Koma panalibe ana a Isiraeli amene Solomo anawasandutsa akapolo ogwira ntchito yake,+ chifukwa iwo anali ankhondo ake,+ atsogoleri a asilikali ake othandiza pamagaleta, atsogoleri a asilikali ake oyendetsa magaleta+ ndiponso a amuna ake okwera pamahatchi.+