Deuteronomo 28:63 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 63 “Chotero, monga mmene Yehova anasangalalira kuti akuchitireni zabwino ndi kukuchulukitsani,+ momwemonso adzasangalala kuti akuwonongeni ndi kukufafanizani.+ Pamenepo mudzatheratu m’dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu.+ 1 Mafumu 14:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Iye adzasiya Isiraeli+ chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita, ndiponso amene anachimwitsa nawo Isiraeli.”+ Hoseya 1:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ndiyeno Yehova anauza Hoseya kuti: “Mwanayu umupatse dzina lakuti Yezereeli,+ pakuti kwatsala kanthawi kochepa kuti ndiimbe Yezereeli* mlandu wokhetsa magazi, mlandu wa nyumba ya Yehu.+ Pamenepo ndidzathetsa ufumu wolamulira nyumba ya Isiraeli,+ Amosi 5:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Pakuti ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kwambiri ndi ku Damasiko,’+ watero Mulungu wa makamu, amene dzina lake ndi Yehova.”+ Mika 1:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Samariya ndidzamusandutsa bwinja+ ndi malo oyenera kubzalapo mpesa. Miyala yake ndidzaiponya m’chigwa ndipo maziko ake ndidzawafukula n’kuwasiya pamtunda.+
63 “Chotero, monga mmene Yehova anasangalalira kuti akuchitireni zabwino ndi kukuchulukitsani,+ momwemonso adzasangalala kuti akuwonongeni ndi kukufafanizani.+ Pamenepo mudzatheratu m’dziko limene mukupita kukalitenga kukhala lanu.+
16 Iye adzasiya Isiraeli+ chifukwa cha machimo amene Yerobowamu anachita, ndiponso amene anachimwitsa nawo Isiraeli.”+
4 Ndiyeno Yehova anauza Hoseya kuti: “Mwanayu umupatse dzina lakuti Yezereeli,+ pakuti kwatsala kanthawi kochepa kuti ndiimbe Yezereeli* mlandu wokhetsa magazi, mlandu wa nyumba ya Yehu.+ Pamenepo ndidzathetsa ufumu wolamulira nyumba ya Isiraeli,+
27 Pakuti ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kwambiri ndi ku Damasiko,’+ watero Mulungu wa makamu, amene dzina lake ndi Yehova.”+
6 Samariya ndidzamusandutsa bwinja+ ndi malo oyenera kubzalapo mpesa. Miyala yake ndidzaiponya m’chigwa ndipo maziko ake ndidzawafukula n’kuwasiya pamtunda.+