6 M’chaka cha 9 cha Hoshiya, mfumu ya Asuri inalanda Samariya+ n’kutenga Aisiraeli kupita nawo ku Asuri.+ Mfumuyo inakaika Aisiraeliwo ku Hala+ ndi ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani,+ ndiponso m’mizinda ya Amedi.+
23 mpaka Yehova anachotsa Isiraeli pamaso pake+ monga momwe ananenera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri.+ Choncho Isiraeli anachoka m’dziko lake n’kupita ku Asuri, ndipo ali komweko mpaka lero.+