Salimo 50:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Pa tsiku la nsautso undiitane.+Ine ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.”+ Salimo 116:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Pakuti watchera khutu lake kwa ine,+Ndipo ndidzaitanira pa iye masiku onse a moyo wanga.+ Yesaya 38:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Atamva mawu amenewa, Hezekiya anatembenukira kukhoma+ n’kuyamba kupemphera kwa Yehova.+ Mateyu 6:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha+ ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka.+ Ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera. Afilipi 4:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse,+ koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero,+ pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.+
6 Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha+ ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka.+ Ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera.
6 Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse,+ koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero,+ pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.+