Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:48
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 48 Udzatumikira adani ako+ amene Yehova adzawatuma kuti akuukire. Udzawatumikira uli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso ukusowa china chilichonse. Adzakuveka goli lachitsulo m’khosi lako kufikira atakufafaniza.+

  • Deuteronomo 29:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 “Pamenepo m’badwo wa m’tsogolo, ana anu amene adzabwera pambuyo panu, ndiponso mlendo amene adzachokera kudziko lakutali, akadzaona miliri ndi nthenda zimene Yehova wakantha nazo dzikolo,+ adzanena mawu.

  • 2 Mafumu 24:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Patapita nthawi, Yehoyakini mfumu ya Yuda anatuluka n’kupita kwa mfumu ya Babulo+ pamodzi ndi mayi ake,+ atumiki ake, akalonga ake, ndi nduna za panyumba yake, ndipo mfumu ya Babuloyo inam’tengera Yehoyakini ku ukapolo m’chaka cha 8+ cha ufumu wake.

  • 2 Mafumu 25:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo+ n’kupita nayo ku Ribila+ kwa mfumu ya Babulo, kuti akaiuze chigamulo chake.

  • 2 Mbiri 33:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Pomalizira pake Yehova anawabweretsera+ akuluakulu a asilikali a mfumu ya Asuri.+ Iwo anagwira Manase akubisala m’dzenje.+ Atatero anam’manga+ ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena