2 Mafumu 21:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+ 2 Mafumu 23:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Komabe Yehova sanabweze mkwiyo wake waukulu umene unayakira Yuda,+ chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene Manase anawachititsa, n’kukwiyitsa nazo Mulungu.+ 2 Mbiri 33:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Pomalizira pake Yehova anawabweretsera+ akuluakulu a asilikali a mfumu ya Asuri.+ Iwo anagwira Manase akubisala m’dzenje.+ Atatero anam’manga+ ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo. 2 Mbiri 33:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva kupembedzera kwake+ ndi pempho lake lopempha chifundo. Kenako anam’bwezera ku Yerusalemu ku ufumu wake,+ ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.+
16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+
26 Komabe Yehova sanabweze mkwiyo wake waukulu umene unayakira Yuda,+ chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene Manase anawachititsa, n’kukwiyitsa nazo Mulungu.+
11 Pomalizira pake Yehova anawabweretsera+ akuluakulu a asilikali a mfumu ya Asuri.+ Iwo anagwira Manase akubisala m’dzenje.+ Atatero anam’manga+ ndi zomangira ziwiri zamkuwa n’kupita naye ku Babulo.
13 Manase anayamba kupemphera kwa Mulungu ndipo iye anamva kupembedzera kwake+ ndi pempho lake lopempha chifundo. Kenako anam’bwezera ku Yerusalemu ku ufumu wake,+ ndipo Manase anadziwa kuti Yehova ndiye Mulungu woona.+