Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Aliyense wokhetsa magazi a munthu, nayenso magazi ake adzakhetsedwa ndi munthu,+ chifukwa Mulungu anapanga munthu m’chifaniziro chake.

  • Numeri 35:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 “‘Musadetse dziko+ limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndiwo amadetsa dziko. Ndipo dziko lodetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe mwa njira ina, koma ndi magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+

  • 2 Mafumu 24:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 komanso chifukwa cha magazi osalakwa+ amene iye anakhetsa, moti anadzaza Yerusalemu ndi magazi osalakwa, ndipo Yehova sanalole kukhululuka.+

  • Miyambo 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Maso odzikweza,+ lilime lonama,+ manja okhetsa magazi a anthu osalakwa,+

  • Yesaya 59:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakuti m’manja mwanu mwaipitsidwa ndi magazi,+ ndipo zala zanu zaipitsidwa ndi zolakwa.+ Milomo yanu yanena zabodza. Lilime lanu limangokhalira kunena zinthu zopanda chilungamo.+

  • Yeremiya 2:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Komanso, pazovala zako papezeka madontho a magazi a anthu+ osauka osalakwa.+ Madontho a magaziwo sindinawapeze panyumba, ngati kuti anali kuthyola nyumbayo, koma ndawapeza pazovala zako zonse.+

  • Mateyu 23:30
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 30 ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako m’masiku a makolo athu, ifeyo sitikanakhudzidwa ndi mlandu wawo wokhetsa magazi a aneneri.’+

  • Aheberi 11:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Anaponyedwa miyala,+ anayesedwa,+ anachekedwa pakati ndi macheka, anaphedwa+ mwankhanza ndi lupanga, anayendayenda atavala zikopa za nkhosa+ ndi zikopa za mbuzi pamene anali osowa,+ pamene anali m’masautso+ komanso pamene anali kuzunzidwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena