16 Manase anakhetsanso magazi osalakwa ochuluka zedi,+ mpaka magaziwo anadzaza nawo Yerusalemu kuyambira koyambirira mpaka kumapeto, kuwonjezera pa tchimo lake limene anachimwitsa nalo Yuda mwa kuchita zoipa pamaso pa Yehova.+
4 Zidzatero chifukwa andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Iwo amaperekanso nsembe zautsi kwa milungu ina imene sanali kuidziwa,+ iwowo, makolo awo ndi mafumu a Yuda, ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+
35 kuti magazi onse olungama okhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu,+ kuyambira magazi a Abele+ wolungama+ mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene inu munamupha pakati pa nyumba yopatulika ndi guwa lansembe.+