Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 “Yehova adzakutumizira matemberero,+ chisokonezo+ ndi chilango+ pa ntchito zako zonse zimene ukuyesa kugwira. Adzakuchitira zimenezi kufikira utafafanizidwa ndi kutha mofulumira, chifukwa cha kuipa kwa zochita zako popeza kuti wandisiya.+

  • 2 Mafumu 22:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 chifukwa chakuti andisiya n’kumakafukiza nsembe yautsi kwa milungu ina+ kuti andikwiyitse ndi ntchito zonse za manja awo.+ Choncho mkwiyo wanga wayakira malo ano ndipo suzimitsidwa.’”’+

  • Yesaya 65:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “Koma anthu inu mwamusiya Yehova.+ Mwaiwala phiri langa loyera.+ Inu mumayalira tebulo mulungu wa Mwayi.+ Mumadzaza chikho ndi vinyo wosakaniza n’kupereka kwa mulungu wa Zokonzedweratu.+

  • Yeremiya 2:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 ‘chifukwa pali zinthu ziwiri zoipa zimene anthu anga achita: Iwo asiya ine+ kasupe wa madzi amoyo,+ ndipo akumba zitsime zawozawo, zitsime zong’ambika zimene sizingasunge madzi.’

  • Yeremiya 15:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “‘Iwe wandisiya,’+ watero Yehova. ‘Ukundifulatira ndi kundichokera.+ Choncho nditambasula dzanja langa kuti ndikukanthe ndi kukuwononga.+ Ndatopa nako kukumvera chisoni.+

  • Yeremiya 17:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Isiraeli,+ onse amene akukusiyani adzachita manyazi.+ Mayina a anthu onse okupandukirani+ adzalembedwa pafumbi chifukwa asiya Yehova magwero a madzi amoyo.+

  • Danieli 9:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Ife tachimwa,+ talakwa, tachita zinthu zoipa ndipo takupandukirani.+ Tapatuka ndiponso tasiya malamulo anu ndi zigamulo zanu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena