6 Koma inuyo ndi ana anu mukadzabwerera n’kusiya kunditsatira,+ osasunga malamulo anga amene ndakupatsani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina+ ndi kuigwadira,
11 Kodi pali mtundu wa anthu umene unasinthanitsapo milungu yawo+ ndi zinthu zimene kwa iwo si milungu yeniyeni?+ Koma anthu anga asinthanitsa ulemerero wanga ndi zinthu zosapindulitsa.+