Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 24:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 M’masiku ake, Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo anabwera kudzachita nkhondo ndi Yerusalemu. Choncho Yehoyakimu anakhala mtumiki wake+ kwa zaka zitatu, koma kenako anam’pandukira.

  • Yeremiya 27:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 “‘“‘Ndiyeno mtundu uliwonse wa anthu ndi ufumu umene sudzatumikira Nebukadinezara mfumu ya Babulo, umenenso sudzaika khosi lake m’goli la mfumu ya Babulo, ine ndidzaulanga ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri+ kufikira nditaufafaniza kudzera mwa Nebukadinezara,’+ watero Yehova.

  • Yeremiya 32:28
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikupereka mzinda uwu m’manja mwa Akasidi ndi m’manja mwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo, ndipo aulanda.+

  • Yeremiya 43:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Inetu ndikuitana Nebukadirezara mfumu ya Babulo+ mtumiki wanga,+ ndipo ndidzaika mpando wake wachifumu pamwamba penipeni pa miyala iyi imene ndaibisa. Iye adzamanga hema wake waulemerero pamwamba pa miyala imeneyi.

  • Ezekieli 26:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidzatumiza Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mfumu ya mafumu,+ kuchokera kumpoto+ kuti akaukire Turo. Iye adzapita ndi mahatchi,+ magaleta ankhondo,+ asilikali a pamahatchi, khamu la anthu+ kapena kuti gulu lalikulu la anthu.

  • Danieli 4:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Uwu ndi uthenga wochokera kwa ine mfumu Nebukadinezara wopita kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana, olankhula zinenero zosiyanasiyana amene akukhala padziko lonse lapansi:+ Mukhale ndi mtendere wochuluka.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena