Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 29:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ine ndidzamanga misasa mokuzungulira mbali zonse kuti ndichite nawe nkhondo. Ndidzamanga mpanda wa mitengo yosongoka mokuzungulira, ndipo ndidzamanga chiunda choti ndidzamenyerepo nkhondo pomenyana nawe.+

  • Yeremiya 32:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pa nthawi imeneyo, magulu ankhondo a mfumu ya Babulo anali atazungulira Yerusalemu.+ Ndipo mneneri Yeremiya anali atamutsekera m’nyumba imene inali m’Bwalo la Alonda.+ Bwalo limeneli linali pafupi ndi nyumba ya mfumu ya Yuda.

  • Yeremiya 37:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ndiyeno gulu lankhondo la Akasidi litabwerera kuchoka ku Yerusalemu+ chifukwa cha gulu lankhondo la Farao,+

  • Yeremiya 52:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 Ndiyeno m’chaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya,+ m’mwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadirezara mfumu ya Babulo pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwera ku Yerusalemu+ kudzaukira mzindawo. Atafika anayamba kumanga misasa ndi khoma kuzungulira mzinda wonsewo.+

  • Ezekieli 4:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Uchite nkhondo ndi mzindawo+ ndipo umange mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira mzinda wonsewo.+ Umangenso chiunda chomenyerapo nkhondo*+ ndi misasa yokhalamo asilikali ankhondo. Uikenso zida zankhondo zowonongera mzindawo kuzungulira mzinda wonsewo.+

  • Ezekieli 21:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 M’dzanja lake lamanja, maulawo asonyeza kuti iye apite ku Yerusalemu, kuti akaike zida zogumulira mzindawo,+ akalamule asilikali ake kuti aphe anthu, akalize chizindikiro chochenjeza,+ akaike zida zogumulira zipata za mzindawo, ndiponso kuti akamange chiunda chomenyerapo nkhondo, ndi mpanda womenyerapo nkhondo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena