Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 20:15
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 15 Anthuwo anafika ndi kumuzungulira ali mumzinda+ wa Abele wa ku Beti-maaka. Iwo anamanga chiunda chomenyerapo nkhondo* ndi mzindawo. Anthu onse amene anali ndi Yowabu anali kukumba pansi pa mpandawo kuti augwetse.

  • Yeremiya 6:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Pakuti Yehova wa makamu wanena kuti: “Dulani mitengo+ kuti tipangire Yerusalemu chiunda chomenyerapo nkhondo.*+ Yerusalemu ndi mzinda woyenera kuimbidwa mlandu.+ Mkati mwake muli kuponderezana kokhakokha.+

  • Yeremiya 32:24
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 24 Taonani! Anthu abwera kumzinda uno ndipo amanga ziunda zomenyerapo nkhondo+ kuti aulande,+ moti uperekedwa m’manja mwa Akasidi amene akumenyana ndi anthu a mumzindawu.+ Anthu adzafa ndi lupanga,+ njala yaikulu+ ndi mliri.+ Zimene munanena zachitika ndipo ndi izi mukuzionazi.+

  • Ezekieli 26:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Anthu okhala m’midzi yozungulira imene ili kunja kwa mzindawu adzawapha ndi lupanga. Iwo adzakumangira mpanda womenyerapo nkhondo ndi chiunda chomenyerapo nkhondo,+ ndipo adzadziteteza ndi chishango chachikulu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena