Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 24:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Atangomaliza ntchitoyo anabweretsa ndalama zotsalazo kwa mfumu ndi Yehoyada. Ndi ndalamazo, iwo anapanga ziwiya za nyumba ya Yehova ndiponso ziwiya zogwiritsira ntchito pa utumiki+ ndi popereka zopereka. Anapanganso makapu+ ndi ziwiya zagolide+ ndi siliva, ndipo nsembe zopsereza+ zinayamba kuperekedwa nthawi zonse m’nyumba ya Yehova masiku onse a Yehoyada.

  • 2 Mbiri 36:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Mfumuyo inatenga ziwiya zonse,+ zazikulu+ ndi zazing’ono, za m’nyumba ya Mulungu woona. Inatenganso chuma+ cha m’nyumba ya Yehova, chuma cha mfumu+ ndi cha akalonga ake. Inatenga chilichonse n’kupita nacho ku Babulo.

  • Ezara 1:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Ziwiya zonse zagolide ndi zasiliva zinalipo 5,400 ndipo Sezibazara+ anabweretsa zonsezi ku Yerusalemu. Anatenganso anthu amene anagwidwa ukapolo+ kuchoka nawo ku Babulo n’kupita nawo ku Yerusalemu.

  • Danieli 5:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Belisazara ataledzera ndi vinyoyo+ anaitanitsa ziwiya zagolide ndi zasiliva+ zimene Nebukadinezara bambo ake anatenga m’kachisi ku Yerusalemu. Anaitanitsa zimenezi kuti mfumuyo, nduna zake, adzakazi* ake ndi akazi ake ena apambali amweremo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena