26Tsopano m’dzikomo munagwanso njala, kuwonjezera pa njala yoyamba ija imene inagwa m’masiku a Abulahamu.+ Choncho Isaki anapita kwa Abimeleki, mfumu ya Afilisiti, ku Gerari.+
1Tsopano zinachitika kuti, m’masiku amene oweruza+ anali atsogoleri, m’dzikomo munagwa njala.+ Ndiyeno munthu wina anasamuka ku Betelehemu+ wa ku Yuda kukakhala m’dziko la Mowabu+ monga mlendo. Anasamuka ndi mkazi wake ndi ana ake awiri aamuna.