9 Usaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,*+ wolanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo,* chifukwa cha zolakwa za anthu odana ndi ine.+
23 Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.+