14 Ali pamenepo, anatenga chovala chauneneri cha Eliya chimene chinagwa chija n’kumenya nacho madzi a mtsinjewo,+ n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?”+ Atamenya madziwo, pang’onopang’ono madziwo anagawanika uku ndi uku, ndipo Elisa anawoloka.