17 Pamenepo Davide anatuluka kukakumana nawo, ndipo anawauza kuti: “Ngati mwabwerera mtendere+ kwa ine kudzandithandiza, mtima wanga ugwirizana nanu.+ Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, pamene sindinalakwe ndi manja anga,+ Mulungu+ wa makolo athu aone zimenezo ndipo aweruze.”+