11 “Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, wabweza mkwiyo wanga+ pa ana a Isiraeli, chifukwa sanalekerere konse zoti anthu azipikisana nane pakati pawo.+ Inetu ndikanawafafanizadi ana a Isiraeliwa, chifukwa ndimafuna kuti azikhala odzipereka kwa ine ndekha basi.+