-
2 Mafumu 11:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Koma wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a magulu a asilikali 100, kapena kuti asilikali osankhidwa,+ kuti: “M’chotseni pakati pa mizere ya anthu! Aliyense amene angam’tsatire pambuyo pake aphedwe ndi lupanga!”+ Popeza wansembeyo anali atanena kuti: “Muonetsetse kuti asaphedwere m’nyumba ya Yehova.”
-
-
2 Mafumu 11:19Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Atatero anauza atsogoleri a magulu a asilikali 100, asilikali olondera mfumu Achikariya,+ asilikali othamanga,+ ndi anthu onse a m’dzikolo, kuti aperekeze mfumuyo kuchokera kunyumba ya Yehova. Anthuwo anadzera njira ya pachipata+ cha asilikali othamanga, mpaka anafika kunyumba ya mfumu. Kenako mfumuyo inakhala pampando wachifumu+ wa mafumu.
-