13 Owerengedwa onse ayenera kupereka zotsatirazi: hafu ya sekeli yolingana ndi sekeli la kumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli limodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+
9 Atatero anauza anthu onse a ku Yuda ndi ku Yerusalemu kuti abweretse kwa Yehova msonkho wopatulika+ umene Mose+ mtumiki wa Mulungu woona analamula Aisiraeli m’chipululu.