26 Iye anatenga chuma cha m’nyumba ya Yehova ndi chuma cha m’nyumba ya mfumu.+ Anatenga chilichonse+ kuphatikizapo zishango zonse zagolide zimene Solomo anapanga.+
26 Pa alonda a pazipatawo panali amuna anayi amphamvu amene anali pa udindo wawo chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Amunawo anali Alevi, ndipo anali kuyang’anira zipinda zodyera+ ndi chuma+ cha m’nyumba ya Mulungu woona.