28 Zitatero, Samueli anamuuza kuti: “Yehova wang’amba+ ndi kuchotsa ufumu wa Isiraeli kwa iwe lero, ndipo adzaupereka kwa mnzako, munthu woyenerera kuposa iwe.+
10 ndi kusamutsa ufumu kuuchotsa m’nyumba ya Sauli, n’kukhazikitsa mpando wachifumu wa Davide mu Isiraeli ndi mu Yuda, kuchokera ku Dani mpaka ku Beere-seba.”+
3 Choncho akulu onse+ a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Mfumu Davide anachita nawo pangano+ ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli.+